4 pakuti ikudza mwacabe, nicoka mumdima, mdima nukwirira dzina lace.
5 Ngakhale dzuwa siliona ngakhale kulidziwa, imeneyi ipambana winayo kupuma;
6 akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita ku malo amodzi?
7 Nchito zace zonse munthu angogwirira m'kamwa mwace, koma mtima wace sukhuta.
8 Pakuti wanzeru ali ndi ciani coposa citsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pa maso pa amoyo ali ndi ciani?
9 Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; icinso ndi cabe ndi kungosautsa mtima.
10 Comwe cinalipo cachedwa dzina lace kale, cidziwika kuti ndiye munthu; sakhoza kulimbana ndi womposa mphamvu.