8 Pakuti wanzeru ali ndi ciani coposa citsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pa maso pa amoyo ali ndi ciani?
9 Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; icinso ndi cabe ndi kungosautsa mtima.
10 Comwe cinalipo cachedwa dzina lace kale, cidziwika kuti ndiye munthu; sakhoza kulimbana ndi womposa mphamvu.
11 Pokhala zinthu zambiri zingocurukitsa zacabe, kodi anthu aona phindu lanji?
12 Pakuti ndani adziwa comwe ciri cabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wace wacabe umene autsiriza ngati mthunzi? pakuti ndani adzauza munthu cimene cidzaoneka m'tsogolo mwace kunja kuno?