14 Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ici pambali pa cinzace, kuti anthu asapeze kanthu ka m'tsogolo mwao.
15 Ndaona zonsezi masiku anga acabe; pali wolungama angofa m'cilungamo cace, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m'kuipa kwace.
16 Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziononga wekha?
17 Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa, uferenji nthawi yako isanafike?
18 Kuli kwabwino kugwira ici; indetu, usacotsepo dzanja lako pakuti yemwe aopa Mulungu adzaturuka monsemo.
19 Nzeru ilimbitsa wanzeru koposa akuru khumi akulamulira m'mudzi.
20 Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene acita zabwino osacimwa.