12 Pakuti munthu sadziwatu mphindi yace; monga nsomba zigwidwa m'ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.
13 Ndaonanso nzeru pansi pano motero, ndipo inandionekera yaikuru;
14 panali mudzi waung'ono muli anthu owerengeka; ndipo inadzako mfumu yaikuru, niizinga ndi nkhondo, nimangapo malinga akuru;
15 koma anapezedwamo mwamuna wanzeru wosauka, yemweyo napulumutsa mudziwo ndi nzeru yace; koma panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo.
16 Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ace.
17 Mau a anzeru acete amveka koposa kupfuula kwa wolamulira mwa zitsiru.
18 Nzeru ipambana zida za nkhondo; koma wocimwa mmodzi aononga zabwino zambiri.