3 Ndinayankha kuti, Ndabvula maraya anga, ndiwabvalenso bwanji?Ndatsuka mapazi anga; ndiwadetserenii?
4 Bwenzi langa analonga dzanja lace pazenera,Mtima wanga ndi kuguguda cifukwa ca iye,
5 Ndinauka ndikatsegulire bwenzi langa;Pamanja panga panakha nipa.Ndi pa zala zanga madzi a nipa, Pa zogwirira za mpikizo,
6 Ndinamtsegulira bwenzi langalo;Koma ndinampeza, bwenzi langa atacoka.Moyo wanga unalefuka polankhula iye:Ndinamfunafuna, osampeza;Ndinamuitana, koma sanandibvomera.
7 Alonda akuyenda m'mudzi anandipeza,Nandikantha, nanditema;Osunga maguta nandicotsera cophimba canga.
8 Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,Mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza ciani?Kuti ndadwala ndi cikondi.
9 Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,Mkaziwe woposa kukongola?Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,Kuti utilumbirira motero?