14 koma cisomo ca Ambuye wathu cidacurukatu pamodzi ndi cikhulupiriro ndi cikondi ciri mwa Kristu Yesu.
15 Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Kristu Yesu anadza ku dziko lapansi kupulumutsa ocimwa; wa iwowa ine ndine woposa;
16 komatu mwa ici anandicitira cifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Kristu akaonetsere kuleza mtima kwace konse kukhale citsanzo ca kwa iwo adzakhulupirira pa iye m'tsogolo kufikira moyo wosatha.
17 Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosabvunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.
18 Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, emonga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino;
19 ndi kukhala naco cikhulupiriro ndi cikumbu mtima cokoma, cimene ena adacikankha, cikhulupiriro cao cidatayika;
20 a iwo ali Humenayo ndi Alesandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano.