4 Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng'ombe zamphongo, ndimbuzi ukacotsera macimo.
5 Mwa ici polowa m'dziko lapansi, anena,Nsembe ndi copereka simunazifuna,Koma thupi munandikonzera Ine.
6 Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa macimo simunakondwera nazo;
7 Pamenepo ndinati, Taonani, ndafika,(Pamutu pace pa buku palembedwa za Ine)Kudzacita cifuniro canu, Mulungu,
8 Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa macimo simunazifuna, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo),
9 pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzacita cifuniro canu. Acotsa coyambaco, kuti akaike caciwirico.
10 Ndi cifuniro cimeneco tayeretsedwa mwa copereka ca thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.