32 Ndipo ndinene cianinso? pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za 5 Gideoni, 6 Baraki, 7 Samsoni, 8 Yefita; za 9 Davide, ndi 10 Samueli ndi aneneri;
33 amene mwa cikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anacita cilungamo, analandira malonjezano, 11 anatseka pakamwa mikango,
34 12 nazima mphamvu ya moto, 13 napulumuka lupanga lakuthwa, 14 analimbikitsidwa pokhala ofok a, anakula mphamvu kunkhondo, 15 anapitikitsa magulu a nkhondo yacilendo.
35 16 Akazi analandira akufa ao mwa kuuka kwa akufa; ndipo 17 ena anakwapulidwa, osalola kuomboledwa,
36 kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi 18 kuwatsekera m'ndende;
37 19 anaponyedwa miyala, anacekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda obvala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ocitidwa zoipa,
38 (amenewo dziko lapansi silinayenera iwo), osokerera m'mapululu, ndi m'mapiri, ndi 20 m'mapanga, ndi m'mauna a dziko.