1 Cikondi ca pa abale cikhalebe.
2 Musaiwale kucereza alendo; pakuti mwa ici ena anacereza angelo osacidziwa.
3 Kumbukilani am'nsinga, monga am'nsinga anzao; ocitidwa zoipa, monga ngati inunso adatero nanu m'thupi.
4 Ukwati ucitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi acigololo adzawaweruza Mulungu.
5 Mtima wanu ukhale wosakonda cuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.
6 Kotero kuti tinena molimbika mtima,Mthandizi wanga ndiye Ambuye; smdidzaopa;Adzandicitira ciani munthu?