20 Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye woturuka mwa akufa 1 Mbusa wamkuru wa nkhosa 2 ndi mwazi wa cipangano cosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,
21 3 akuyeseni inu opanda cirema m'cinthu ciri conse cabwino, kuti mucite cifuniro cacej ndi kucita mwa ife comkondweretsa pamaso pace, mwa Yesu Kristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen.
22 Koma ndidandaulira inu, abale, lolani mau acidandauliro; pakutinso ndalembera inu mwacidule.
23 Zindikirani kuti mbale wathu 4 Timoteo wamasulidwa; pamodzi ndi iye, ngati akudza msanga, ndidzakuonani inu.
24 Lankhulani 5 atsogoleri anu onse, ndi oyera mtima onse. Akulankhulani iwo a ku Italiya.
25 Cisomo cikhale ndi inu nonse. Amen.