7 alangizanso tsiku lina, ndi kunena m'Davide, itapita nthawi yaikuru yakuti, Lero, monga kwanenedwakale,Lero ngati mudzamva mau ace,Musaumitse mitima yanu.
8 Pakuti ngati Yoswa akadawapumitsa iwo, sakadalankhuia m'tsogolomo za tsiku lina.
9 Momwemo utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu.
10 Pakuti iye amene adalowa mpumulo wace, adapumulanso mwini wace ku nchito zace, monganso Mulungu ku zace za iye.
11 Cifukwa cace ticite cangu ca kulowa mpumulowo, kuti f winaangagwe m'citsanzo comwe ca kusamvera.
12 Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ocitacita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.
13 Ndipo palibe colengedwa cosaonekera pamaso pace, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zobvundukuka pamaso pace pa iye amene ticita naye.