6 Koma tsopano iye walandira citumikiro comveka coposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.
7 Pakuti loyamba lija likadakhala lopanda cirema sakadafuna malo a laciwirilo.
8 Pakuti powachulira iwo cifukwa, anena,Taonani, akudza masiku, anena Ambuye,Ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda,
9 Losati longa pangano ndinalicita ndi makolo ao,Tsikuli ndinawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera aturuke m'dziko la Aigupto;Kuti iwo sanakhalabe m'pangano langa,Ndipo loe sindinawasamalira iwo, anena Ambuye,
10 Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israyeli,Atapita masiku ajawa, anena Ambuye:Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m'nzeru zao,Ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo;Ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu,Ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu:
11 Ndipo sadzaphunzitsa yense mfulu mnzace,Ndipo yense mbale wace, ndi kuti, Zindikira Ambuye:Pakuti onse adzadziwa Ine, Kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru wa iwo.
12 Kuti ndidzacitira cifundo rosalungama zao,Ndipo zoipa zao sindidzazikumbukanso.