8 ndipo ndidzalikha okhala m'Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yacifumu m'Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.
9 Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Turo, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukila pangano lacibale;
10 koma ndidzatumiza moto pa linga la Turo, ndipo udzanyeketsa nyumba zace zacifumu.
11 Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza analondola mphwace ndi lupanga, nafetsa cifundo cace conse, ndi mkwiyo wace unang'amba cing'ambire, nasunga mkwiyo wace cisungire;
12 koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zacifumu za Bozira.
13 Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Gileadi, kuti akuze malire ao;
14 koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zacifumu zace, ndi kupfuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kabvumvulu;