2 Inu nokha ndinakudziwani mwa mabanja onse a pa dziko lapansi, m'mwemo ndidzakulangani cifukwa ca mphulupulu zanu zonse.
3 Kodi awiri adzayenda pamodzi asanapanganiranetu?
4 Kodi mkango udzabangula m'nkhalango wosakhala nayo nyama? Kodi msona wa mkango udzalira m'ngaka mwace usanagwire kanthu?
5 Kodi mbalame idzakodwa mumsampha pansi popanda msampha woichera? Kodi msampha ufamphuka pansi wosakola kanthu?
6 Kodi adzaomba lipenga m'mudzi osanieniemera anthu? Kodi coipa cidzagwera mudzi osacicita Yehova?
7 Pakuti Ambuye Yehova sadzacita kanthu osaulula cinsinsi cace kwa atumiki ace aneneri.
8 Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?