1 Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basana, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani naco, timwe.
2 Ambuye Yehova walumbira pali ciyero cace, kuti taonani, adzakugwerani masiku akuti adzakucotsani ndi zokowera, ndi otsala anu ndi mbedza.
3 Ndipo mudzaturukira popasuka linga, yense m'tsogolo mwace, ndi kutayika ku Harimoni, ati Yehova.
4 Idzani ku Beteli, mudzalakwe ku Giligala, nimucurukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m'mawa ndi m'mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatu atatu;