6 Ndipo ine ndakupatsaninso mano oyera m'midzi yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.
7 Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinabvumbistira mudzi umodzi mvula, osabvumbitsira mudzi wina; munda wina unabvumbidwa mvula, ndi m'munda mosabvumbidwa mvula munafota.
8 M'mwemo midzi iwiri kapena itatu inayenda peyupeyu ku mudzi umodzi kukamwa madzi, koma sanakhuta; koma simunai bwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.
9 Ndinakukanthani ndi cinsikwi ndi cinoni; minda yanu yocuruka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi yaazitona, yaonongeka ndi cirimamine; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.
10 Ndinatumiza mliri pakati panu monga m'Aigupto; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa cigono canu kufikitsa kumphuno kwanu; ikoma simunabwerera kudzakwa Ine, ati Yehova.
11 Ndinagubuduza ena mwa inu, monga umo Mulungu anagubuduzira Sodomu ndi Gomora; ndipo inu munali ngati muuni wofumulidwa kumoto; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.
12 Cifukwa cace ndidzatero nawe, Israyeli; popeza ndidzakucitira ici, dzikonzeretu kukomana ndi Mulungu wako, Israyeli.