1 Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.
2 Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lacitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pace.
3 Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kuturuka kwace kwakonzekeratu ngati matanda kuca; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.
4 Efraimu iwe, ndidzakucitira ciani? Yuda iwe, ndikucitire ciani? pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.
5 Cifukwa cace ndawalikha mwa aneneri; ndawapha ndi mau a pakamwa panga; ndi maweruzo anga aturuka ngati kuunika.