1 Usakondwera, Israyeli, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wacita cigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya cigololo pa dwale la tirigu liri lonse.
2 Dwale ndi coponderamo mphesa sizidzawadyetsa, vinyo watsopano adzamsowa.
3 Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efraimu adza bwerera kumka ku Aigupto; ndipo adzadya cakudya codetsa m'Asuri.
4 Sadzatsanulira Yehova nsembe zavinyo; sizidzamkomera Iye nsembe zao; zidzakhala kwa iwo ngati mkate wa acisoni; onse akudyako adzadetsedwa; pakuti mkate wao udzakhala wa njala yao, uwu sudzalowa m'nyumbaya Yehova.
5 Mudzacitanji tsiku la masonkhano oikika, ndi tsiku la madyerero a Yehova?
6 Pakuti taonani, anacokera cionongeko, koma Aigupto adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao.
7 Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israyeli adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, cifukwa ca kucuruka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukuru.