1 Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri.
2 Gawira asanu ndi awiri ngakhale asanu ndi atatu; pakuti sudziwa coipa canji cidzaoneka pansi pano.
3 Mitambo ikadzala mvula, itsanulira pansi; mtengo ukagwa kumwela pena kumpoto, pomwe unagwa mtengowo udzakhala pomwepo.
4 Woyang'ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.
5 Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa nchito za Mulungu amene acita zonse.