4 Woyang'ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.
5 Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa nchito za Mulungu amene acita zonse.
6 Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.
7 Indetu kuunika nkokoma, maso napeza bwino m'kuona dzuwa.
8 Inde, munthu akakhala ndi moyo zaka zambiri, akondwere ndi zonsezo; koma akumbukire masiku amdima kuti adzacuruka. Zonse zirinkudza ziri zacabe.
9 Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.
10 Cifukwa cace cotsani zopweteka m'mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako; pakuti ubwana ndi unyamata ngwa cabe.