1 Pali coipa ndaciona kunja kuno cifalikira mwa anthu,
2 munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa cuma ndi ulemu, mtima wace susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ici ndi cabe ndi nthenda yoipa,
3 Cinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zace ndi kucuruka, koma mtima wace osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo;
4 pakuti ikudza mwacabe, nicoka mumdima, mdima nukwirira dzina lace.
5 Ngakhale dzuwa siliona ngakhale kulidziwa, imeneyi ipambana winayo kupuma;
6 akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita ku malo amodzi?