17 Pfuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Midzi yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.
18 Ndipo ndinakweza maso anga, ndinapenya, taonani, nyanga zinai.
19 Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israyeli, ndi Yerusalemu.
20 Ndipo Yehova anandionetsa osula anai.
21 Pamenepo ndinati, Adzeranji awa? Ndipo ananena, nati, Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, wopandanso wina woweramutsa mutu wace; koma awa anadza kuziopsa, kugwetsa nyanga za amitundu, amene anakwezera dziko la Yuda nyanga zao kulimwaza.