6 Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, ku dzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwace, m'Yerusalemu.
7 Ndipo Yehova adzayamba kupulumutsa mahema a Yuda, kuti ulemerero wa nyumba ya Davide ndi ulemerero wa okhala m'Yerusalemu usakulire Yuda.
8 Tsiku ilo Yehova adzacinjiriza okhala m'Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao.
9 Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ndidzayesa kuononga amitundu onse akudza kuyambana ndi Yerusalemu.
10 Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala m'Yerusalemu, mzimu wa cisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wace mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wace woyamba.
11 Tsiku lomwelo kudzakhala maliro akuru m'Yerusalemu, ngati maliro a Hadadirimoni m'cigwa ca Megidoni,
12 Ndipo dziko lidzalira, banja liri lonse pa lokha; banja la nyumba ya Davide pa lokha, ndi akazi ao pa okha; banja la nyumba ya Natani pa lokha, ndi akazi ao pa okha;