1 Taonani likudza tsiku la Yehova, limene zofunkha zako zidzagawanika pakati pako.
2 Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndi Yerusalemu; ndipo mudziwo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mudzi lidzaturuka kumka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m'mudzimo.
3 Pamenepo Yehova adzaturuka, nadzacita nkhondo ndi amitundu aja, monga anacitira nkhondo tsiku lakudumana.
4 Ndi mapazi ace adzaponda tsiku lomwelo pa phiri la Azitona, liri pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala cigwa cacikuru; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwela.
5 Pamenepo mudzathawa kudzera cigwa ca mapiri anga; pakuti cigwa ca mapiri cidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira cibvomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu.