6 Ndipo ndinati, Nciani ici? Nati iye, Ici ndi efa alikuturuka. Natinso, Ici ndi maonekedwe ao m'dziko lonse;
7 (ndipo taonani, cozunguniza cantobvu cotukulidwa) ndipo ici ndi mkazi wokhala pakati pa efa.
8 Ndipo anati, Uyu ndi ucimo; namgwetsa m'kati mwa efa; naponya ntobvu wolemerawo pakamwa pace.
9 Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anaturuka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a cumba, nanyamula efayo pakati pa dziko ndi thambo.
10 Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Amenewa amuka naye kuti efayo?
11 Ndipo anati kwa ine, Kummangira nyumba m'dziko la Sinara; kuti amuike, namkhazikeko pa kuzika kwace.