6 Atero Yehova wa makamu: Cikakhala codabwitsa pamaso pa otsala a anthu awa masiku awo, kodi cidzakhalanso codabwitsa pamaso panga? ati Yehova wa makamu.
7 Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m'dziko la kum'mawa, ndi m'dziko la kumadzulo;
8 ndipo ndidzabwera nao, nadzakhala m'kati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenso ndidzakhala Mulungu wao, m'coonadi ndi m'cilungamo.
9 Atero Yehova wa makamu: Alimbike manja anu, inu akumva masiku ano mau awa pakamwa pa aneneri amene anakhalako tsiku lakuikidwa maziko a nyumba ya Yehova wa makamu, ndiyo Kacisi, kuti amangidwe.
10 Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakuturuka, kapena wakulowa, cifukwa ca wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzace.
11 Koma tsopano sindidzakhala kwa otsala a anthu awa monga momwe ndinakhalira masiku oyamba, ati Yehova wa makamu.
12 Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zace, ndi nthaka idzapatsa zobala zace, ndi miyamba Idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, cikhale colowa cao.