9 Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundu mitundu, ndi acilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi cisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindula nazo.
10 Tiri nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira cihema alibe ulamuliro wa kudyako.
11 Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa ndi mkulu wa ansembe kulowa m'malo opatulidwa, cifukwa ca zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa.
12 Mwa ici Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa iye yekha, adamva cowawa kunja kwa cipata.
13 Cifukwa cace titurukire kwa iye kunja kwa tsasa osenza thonzo lace.
14 Pakuti pano tiribe mudzi wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.
15 Potero mwa iye tipereke ciperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo cipatso ca milomo yobvomereza dzina lace.