1 Pakuti Melikizedeke uyu, Mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa,
2 amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali Mfumu ya cilungamo, pameneponso Mfumu ya Salemu, ndiko, Mfumu ya mtendere;
3 wopanda atate wace, wopanda amace, wopanda mawerengedwe a cibadwidwe cace, alibe ciyambi ca masiku ace kapena citsiriziro ca moyo wace, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.
4 Koma tapenyani ukulu wace wa iyeyu, amene Abrahamu, kholo lalikuru, anampatsa limodzi la magawo khumi la zosankhika za kunkhondo.
5 Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira nchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa cilamulo, ndiko kwa abaleao, angakhale adaturuka m'cuuno ca Abrahamu;
6 koma iye amene mawerengedwe a cibadwidwe cace sacokera mwa iwo, anatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene ali nao malonjezano.
7 Ndipo popanda citsutsano konse wamng'ono adalitsidwa ndi wamkuru.