2 Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa cihema coona, cimene Ambuye anacimanga, si munthu ai.
3 Pakuti mkulu wa ansembe ali yense aikidwa kupereka mitulo, ndiponso nsembe; potero nkufunika kuti ameneyo akhale nako kanthunso kakupereka,
4 Ndipo iye akadakhala padziko, sakadakhala konse wansembe, popeza pali iwo akupereka mitulo monga mwa lamulo;
5 amene atumikira cifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose acenjezedwa m'mene anafuna kupanga cihema: pakuti, Cenjera, ati, ucite zonse monga mwa citsanzoco caonetsedwa kwa iwe m'phiri.
6 Koma tsopano iye walandira citumikiro comveka coposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.
7 Pakuti loyamba lija likadakhala lopanda cirema sakadafuna malo a laciwirilo.
8 Pakuti powachulira iwo cifukwa, anena,Taonani, akudza masiku, anena Ambuye,Ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda,