8 Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo ku malo opatulika siinaonetsedwe, pokhala cihema coyamba ciri ciriri;
9 ndico ciphiphiritso ca ku nthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za cikumbu mtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.
10 Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyana-siyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.
11 Koma atafika Kristu, Mkuluwansembe wa zokoma zirinkudza, mwa cihema cacikuru ndi cangwiro coposa, cosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, cosati ca ciiengedweici,
12 kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi ana a ng'ombe, koma mwa mwazi wa iye yekha, analowa kamodzi ku malo opatulika, atalandirapo ciombolo cosatha.
13 Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng'ombe zamphongo, ndi makala a ng'ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa, upatutsa kufikira ciyeretso ca thupi;
14 koposa kotani nanga mwazi wa Kristu amene anadzipereka yekha wopanda cirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa cikumbu mtima canu kucisiyanitsa ndi nchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?