3 Ndipo mfumu inauza Asipenazi mkuru wa adindo kuti abwere nao ena a ana a Israyeli, a mbeu ya mafumu, ndi ya akalonga;
4 anyamata opanda cirema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ocenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'cinyumba ca mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Akasidi.
5 Ndipo mfumu inawaikira gawo la cakudya ca mfumu tsiku ndi tsiku, ndi la vinyo wakumwa iye, ndi kuti awalere zaka zitatu, kuti potsiriza pace aimirire pamaso pa mfumu.
6 Mwa awa tsono munali a ana a Yuda, Danieli, Hananiya, Misayeli, ndi Azariya.
7 Ndi mkuru wa adindo anawapatsa maina ena; Danieli anamucha Belitsazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaeli, Mesaki; ndi Azariya, Abedinego.
8 Koma Danieli anatsimikiza mtimti kuti asadzidetse ndi cakudya ca mfumu, kapena ndi vinyo amamwa; cifukwa cace anapempha mkuru wa adindo amlole asadzidetse.
9 Ndipo Mulungu anamkometsera Danieli mtima wa mkuru wa adindo, amcitire cifundo.