1 Caka cacitatu ca Koresi mfumu ya Perisiya, cinabvumbulutsidwa cinthu kwa Danieli, amene anamucha Belitsazara; ndipo cinthuco ncoona, ndico nkhondo yaikuru; ndipo anazindikira cinthuco, nadziwa masomphenyawo.
2 Masiku aja ine Danieli ndinali kulira masabata atatu amphumphu,
3 Cakudya cofunika osacidya ine, nyama kapena vinyo zosapita pakamwa panga, osadzola ine konse, mpaka anakwaniridwa masabata atatu amphumphu,
4 Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi woyamba, pokhala ine m'mphepete mwa mtsinje waukuru, ndiwo Hidikeli,
5 ndinakweza maso anga, ndinapenya ndi kuona munthu wobvala bafuta, womanga m'cuuno ndi golidi woona wa ku Ufazi;
6 thupi lace lomwe linanga berulo, ndi nkhope yace ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ace ngati nyali zamoto, ndi manja ace ndi mapazi ace akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ace kunanga phokoso la aunyinji.
7 Ndipo ine Danieli ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaona masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukuru, nathawa kubisala.