10 Akasidi anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu pa dziko lapansi wokhoza kuulula mlandu wa mfumu; cifukwa cace palibe mfumu, mkuru, kapena wolamulira, wafunsira cinthu cotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Akasidi ali onse.
11 Pakuti cinthu acifuna mfumu ncapatali; ndipo palibe wina wokhoza kuciulula pamaso pa mfumu, koma milungu imene kwao sikuli pamodzi ndi anthu.
12 Cifukwa cace mfumu inakwiya, nizaza kwambiri, nilamulira kuti awaphe anzeru onse m'Babulo.
13 M'mwemo cilamuliroco cidamveka, ndi eni nzeru adati aphedwe; anafuna-funanso Danieli ndi anzace aphedwe.
14 Pamenepo Danieli anabweza mau a uphungu wanzeru kwa Arioki mkuru wa olindirira a mfumu, adaturukawo kukapha eni nzeru a ku Babulo;
15 anayankha nati kwa Arioki mkuru wa olindirira a mfumu, Cilamuliro ca mfumu cifulumiriranji? Pamenepo Arioki anadziwitsa Danieli cinthuci.
16 Nalowa Danieli, nafunsa mfumu amuikire nthawi, kuti aululire mfumu kumasulira kwace.