2 Pamenepo mfumu inauza munthu aitane alembi, ndi openduza, ndi aula, ndi Akasidi, amuululire mfumu maloto ace. Nalowa iwo, naimirira pamaso pa mfumu.
3 Niti nao mfumu, Ndalota loto, nubvutika mzimu wanga kudziwa lotolo.
4 Pamenepo Akasidi anati kwa mfumu m'Ciaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo cikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwace.
5 Niyankha mfumu, niti kwa Akasidi, Candicokera cinthuci; mukapanda kundidziwitsa lotoli ndi tanthauzo lace, mudzadulidwa nthuli nthuli, ndi nyumba zanu zidzayesedwa dzala.
6 Koma mukandidziwitsa lotoli, ndi kumasulira kwace, mudzalandira kwa ine mphatso, ndi mphotho, ndi ulemu waukuru; cifukwa cace mundidziwitse lotoli ndi kumasulira kwace.
7 Nabwerezanso iwo kuyankha, nati, Mfumu ifotokozere anyamata ace lotoli, ndipo tidzaidziwitsa kumasulira kwace.
8 Mfumu inayankha, niti, Ndidziwatu kuti mukunkhuniza dala, pakuona inu kuti cinthuci candicokera.