5 Niyankha mfumu, niti kwa Akasidi, Candicokera cinthuci; mukapanda kundidziwitsa lotoli ndi tanthauzo lace, mudzadulidwa nthuli nthuli, ndi nyumba zanu zidzayesedwa dzala.
6 Koma mukandidziwitsa lotoli, ndi kumasulira kwace, mudzalandira kwa ine mphatso, ndi mphotho, ndi ulemu waukuru; cifukwa cace mundidziwitse lotoli ndi kumasulira kwace.
7 Nabwerezanso iwo kuyankha, nati, Mfumu ifotokozere anyamata ace lotoli, ndipo tidzaidziwitsa kumasulira kwace.
8 Mfumu inayankha, niti, Ndidziwatu kuti mukunkhuniza dala, pakuona inu kuti cinthuci candicokera.
9 Koma mukapanda kundidziwitsa lotoli, mlandu wanu ndi umodzi; popeza mwapanganiranatu mau onama ndi oipa, kuwanena pamaso panga, mpaka idzasanduka nyengo; cifukwa cace mundifotokozere lotoli, momwemo ndidzadziwa kuti mudzandidziwitsa kumasulira kwace komwe.
10 Akasidi anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu pa dziko lapansi wokhoza kuulula mlandu wa mfumu; cifukwa cace palibe mfumu, mkuru, kapena wolamulira, wafunsira cinthu cotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Akasidi ali onse.
11 Pakuti cinthu acifuna mfumu ncapatali; ndipo palibe wina wokhoza kuciulula pamaso pa mfumu, koma milungu imene kwao sikuli pamodzi ndi anthu.