5 kuti pakumva inu mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ngoli, ndi zoyimbitsa ziri zonse, mugwadire ndi kulambira fano lagolidi adaliimika mfumu Nebukadinezara;
6 ndipo ali yense wosagwadira ndi kulambira, adzaponyedwa nthawi yomweyo m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.
7 Potero nthawi yomweyo pakumva anthu onse mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ndi zoyimbitsa ziri zonse, anthu onse, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, anagwadira, nalambira fano lagolidi adaliimika mfumu Nebukadinezara.
8 Cifukwa cace anayandikira Akasidi ena nthawi yomweyi, naneneza Ayuda.
9 Anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Mfumu, mukhale ndi moyo cikhalire.
10 Inu mfumu mwalamulira kuti munthu ali yense amene adzamva mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ngoli, ndi zoyimbitsa ziri zonse, agwadire, nalambire fanolo lagolidi;
11 ndi yense wosagwadira ndi kulambiraadzaponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.