10 Masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga ndi awa: Ndinapenya ndi kuona mtengo pakati pa dziko lapansi, msinkhu wace ndi waukuru.
11 Mtengowo unakula, nulimba, ndi msinkhu wace unafikira kumwamba, nuonekera mpaka cilekezero ca dziko lonse lapansi.
12 Masamba ace anali okoma, ndi zipatso zace zinacuruka, ndi m'menemo munali zakudya zofikira onse, nyama za kuthengo zinatsata mthunzi wace, ndi mbalame za m'mlengalenga zinafatsa m'thambi zace, ndi nyama zonse zinadyako.
13 Ndinaona m'masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba.
14 Anapfuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zace, yoyolani masamba ace, mwazani zipatso zace, nyama zicoke pansi pace, ndi mbalame pa nthambi zace.
15 Koma siyani citsa ndi mizu yace m'nthaka, comangidwa ndi mkombero wa citsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo; ncokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lace likhale pamodzi ndi nyama ziri m'macire a m'dziko.
16 Mtima wace usandulike, usakhalenso mtima wa munthu, apatsidwe mtima wonga wa nyama, nizimpitire nthawi zisanu ndi ziwiri.