23 Pakuyamba iwe mapembedzero ako, linaturuka lamulo; ndipo ndadza ine kukufotokozera; pakuti ukondedwa kwambiri; zindikira tsono mau awa, nulingirire masomphenyawo.
24 Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu amtundu wako ndi mudzi wako wopatulika, kumariza colakwaco, ndi kutsiriza macimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa cilungamo cosalekeza, ndi kukhomera cizindikilo masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulikitsa.
25 Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kuturuka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi chemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mabvuto.
26 Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mudzi ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwace kudzakhala kwa cigumula, ndi kufikira cimariziro kudzakhala nkhondo; cipasuko calembedweratu.
27 Ndipo iye adzapangana cipangano colimba ndi ambiri sabata limodzi; ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa; ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira cimariziro colembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo.