Estere 6 BL92

Ahaswero aona cifukwa ca kucitira Moredekai ulemu

1 Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu.

2 Napeza mudalembedwa kuti Moredekai adaulula za Bigitana ndi Teresi, awiri a adindo a mfumu osunga pakhomo, amene adayesa kumthira manja mfumu Ahaswero.

3 Niti mfumu, Anamcitira Moredekai ulemu ndi ukulu wotani cifukwa ca ici? Ndipo anyamata a mfumu akuitumikira ananena nayo, Sanamcitira kanthu.

4 Niti mfumu, Ali kubwalo ndani? Koma Hamani adalowa m'bwalo lakunja la nyumba ya mfumu kulankhula ndi mfumu za kupacika Moredekai pamtengo adaukonzeratu.

5 Ndipo anyamata a mfumu ananena nayo, Taonani, Hamani alikuima pabwalo. Niti mfumu, Alowe.

6 Nalowa Hamani. Ndipo mfumu inati kwa iye, Kodi amcitire ciani munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu? Ndipo Hamani anati mumtima mwace, Ndaniyo mfumu ikondwera kumcitira ulemu koposa ine?

7 Nati Hamani kwa mfumu, Munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu,

8 amtengere cobvala cacifumu amacibvala mfumu, ndi kavalo amakwerapo mfumu, naike korona wacifumu pamutu pace,

9 napereke cobvala ndi kavalo m'dzanja la wina womveketsa wa akalonga a mfumu, nabveke naco munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu, namuyendetse pa kavaloyo m'khwalala la m'mudzi, napfuule pamaso pace, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu.

10 Pamenepo mfumu inati kwa Hamani, Fulumira, tenga cobvala ndi kavalo monga umo wanenera, nucitire cotero Moredakai Myudayo, wokhala pa cipata ca mfumu; kasasowepo kanthu ka zonse wazinena.

11 Ndipo Hamani anatenga cobvala ndi kavalo, nabveka Moredekai, namuyendetsa pa kavalo m'khwalala la m'mudzi, napfuula pamaso pace, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu.

12 Ndipo Moredekai anabweranso ku cipata ca mfumu. Koma Hamani anafulumira kumka kwao, wacisoni ndi wopfunda mutu wace.

13 Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wace, ndi mabwenzi ace onse, zonse zidamgwera, Nanena naye anzeru ace, ndi Zeresi mkazi wace, Moredekai amene wayamba kutsika pamaso pace, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamlaka; koma udzagwada pamaso pace.

14 Akali cilankhulire naye, anafika adindo a mfumu, nafulumira kumtenga Hamani kumka naye kumadyerero adawakonzera Estere.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10