Estere 1 BL92

Madyerero a Ahaswero

1 IZI zinacitika masiku a Ahaswero, ndiye Ahasweroyo anacita ufumu kuyambira Indiya kufikira Kusi, pa maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri.

2 Masiku ajawo, pokhala Ahaswero pa mpando wa ufumu wace uli m'cinyumba ca ku Susani,

3 caka cacitatu ca ufumu wace, anakonzera madyerero akalonga ace onse, ndi omtumikira; amphamvu a Perisiya ndi Mediya, omveka ndi akalonga a maikowo anakhala pamaso pace,

4 pamene anaonetsa zolemera za ufumu wace waulemu, ndi ulemerero wa ukulu wace woposa, masiku ambiri, ndiwo masiku zana limodzi, mphambu makumi asanu ndi atatu.

5 Atatha masikuwa, mfumu inakonzera madyerero anthu onse okhala m'cinyumba ca ku Susani, akulu ndi ang'ono, masiku asanu ndi awiri, ku bwalo la munda wa maluwa wa ku cinyumba ca mfumu;

6 panali nsaru zolenjeka zoyera, zabiriwiri, ndi zamadzi, zomangika ndi zingwe za thonje labafuta, ndi lofiirira, pa zigwinjiri zasiliva, ndi nsanamira zansangalabwi; makama anali a golidi ndi siliva pa mayalidwe a miyala yofiira, ndi yoyera, ndi yoyezuka, ndi yakuda.

7 Nawapatsa cakumwa m'zomwera zagolidi, zomwerazo nzosiyana-siyana, ndi vinyo wacifumu anacuruka, monga mwa ufulu wa mfumu.

8 Ndi mamwedwewo anali monga mwa lamulo; panalibe kukakamiza; pakuti mfumu idaikira akulu onse a nyumba yace motero, kuti acite monga momwe akhumba ali yense.

Vasiti akana kuoneka kumadyerero

9 Vasiti yemwe, mkazi wamkuru, anakonzera akazi madyerero m'nyumba yacifumu ya mfumu Ahaswero.

10 Tsiku lacisanu ndi ciwiri, pokondwera mtima wa mfumu ndi vinyo, iye anauza Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, ndi Abagita, Zetara, ndi Karikasi, adindo asanu ndi awiriwo akutumikira pamaso pa mfumu Ahaswero,

11 abwere naye Vasiti mkazi wamkuru pamaso pa mfumu ndi korona wacifumu, kuonetsa anthu ndi akuru kukoma kwace; popeza anali wokongola maonekedwe ace.

12 Koma Vasiti mkazi wamkuruyo anakana kudza pa mau a mfumu adamuuza adindowo; potero mfumu idapsa mtima ndithu, ndi mkwiyo wace unatentha m'kati mwace.

Vasiti acotsedwa

13 Pamenepo mfumu inanena kwa eni nzeru, akudziwa za m'tsogolo, mfumu idafotero nao onse akudziwa malamulo ndi maweruzo,

14 a pafupi naye ndiwo Karisena. Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena, ndi Memukana, akalonga asanu ndi awiri a Perisiya ndi Mediya, openya nkhope ya mfumu ndi kukhala oyamba m'ufumu.

15 Anati, Tidzacitanji naye mkazi wamkuru Vasiti monga mwa malamulo, popeza sanacita comuuza mfumu Ahaswero mwa adindo?

16 Ndi Memukana anati pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkuru sanalakwira mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m'maiko onse a mfumu Ahaswero.

17 Pakuti macitidwe awa a mkazi wamkuruyo adzabuka kufikira akazi onse, kupeputsa amuna ao pamaso pao; anthu akati, Mfumu Ahaswero anati abwere naye Vasiti mkazi wamkuru pamaso pace, koma sanadza iye.

18 Inde tsiku lomwelo akazi akuru a Perisiya ndi Mediya, atamva macitidwe a mkazi wamkuruyo, adzatero nao momwemo kwa akalonga onse a mfumu. Ndi cipeputso ndi mkwiyo zidzacuruka.

19 Cikakomera mfumu, aturuke mau acifumu pakamwa pace, nalembedwe m'malamulo a Aperisiya ndi Amediya, angasinthike, kuti Vasiti asalowenso pamaso pa mfumu Ahaswero; ndi mfumu aninkhe cifumu cace kwa mnzace womposa iye.

20 Ndipo mau amene adzaika mfumu akamveka m'ufumu wace wonse, (pakuti ndiwo waukuru), akazi onse adzacitira amuna ao ulemu, akulu ndi ang'ono.

21 Ndipo mauwo anakonda mfumu ndi akalonga; ndi mfumu inacita monga mwa mau a Memukana,

22 natumiza akalata ku maiko onse a mfumu, ku dziko liri lonse monga mwa cilembedwe cao, ndi ku mtundu uli wonse monga mwa cinenedwe cao, kuti mwamuna ali yense akhale wamkuru m'nyumba yace yace, nawabukitse monga mwa cinenedwe ca anthu amtundu wace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10