Estere 5 BL92

Estere alowa kwa mfumu nampempha iye ndi Hamani azidya naye

1 Ndipo kunali tsiku lacitatu, Estere anabvala zobvala zace zacifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wace wacifumu m'nyumba yacifumu, pandunji polowera m'nyumba.

2 Ndipo kunali, pamene mfumu inaona Estere mkazi wamkuruyo alikuima m'bwalo, inamkomera mtima; ndi mfumu inamloza Estere ndi ndodo yacifumu yagolidi inali m'dzanja lace. Nayandikira Estere, nakhudza nsonga ya ndodoyo.

3 Ninena naye mfumu, Mufunanji, Estere mkazi wamkuru? pempho lanu nciani? lidzaperekedwa kwa inu, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.

4 Ndipo Estere anati, Cikakomera mfumu, adze mfumu ndi Hamani lero ku madyerero ndinawakonzera.

5 Niti mfumu, Mumfulumize Hamani, acitike mau a Estere. Nidza mfumu ndi Hamani ku madyerero adawakonzera Estere.

6 Ndipo mfumu inati kwa Estere pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nciani? lidzaperekedwa kwa inu; mufunanji? cidzacitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.

7 Nayankha Estere, nati, Pempho langa ndi kufuna kwanga ndiko,

8 ngati mfumu indikomera mtima, ngatinso cakomera mfumu kupereka pempho langa ndi kucita cofuna ine, adze mfumu ndi Hamani ku madyerero ndidzawakonzera; ndipo mawa ndidzacita monga yanena mfumu.

Hamani amangitsa popacika Moredekai

9 Ndipo Hamani anaturuka tsiku lomwelo wosekerera ndi wokondwera mtima; koma pamene Hamani anapenya Moredekai ku cipata ca mfumu, osamnyamukira kapena kumfumukira, Hamani anadzazidwa ndi mkwiyo pa Moredekai.

10 Koma Hamani anadziletsa, namuka kwao, natumiza munthu kukatenga mabwenzi ace, ndi Zeresi mkazi wace.

11 Nawawerengera Hamani kulemera kwace kwakukuru, ndi ana ace ocuruka, ndi zonse mfumu idamkuza nazo, ndi umo adamkweza koposa akalonga ndi anyamata a mfumu.

12 Hamani anatinso, Ndiponso Estere mkazi wamkuru sanalola mmodzi yense alowe pamodzi ndi mfumu ku madyerero adakonzawo, koma ine ndekha; nandiitana mawanso pamodzi ndi mfumu.

13 Koma zonsezi sindipindula nazo kanthu konse, pokhala ndirikuona Moredekai Myudayo alikukhala ku cipata ca mfumu.

14 Pamenepo Zeresi mkazi wace, ndi mabwenzi ace onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wace mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampacike Moredekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ici cidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10