Estere 2 BL92

Ahaswero akwatira Estere

1 Zitatha izi, utaleka mkwiyo wa mfumu Ahaswero, anakumbukila Vasiti, ndi cocita iye, ndi comlamulidwira.

2 Pamenepo anyamata a mfumu omtumikira anati, Amfunire mfumu anamwali okongola;

3 ndi mfumu aike oyang'anira m'maiko onse a ufumu wace, kuti asonkhanitse anamwali onse okongola m'cinyumba ca ku Susani, m'nyumba ya akazi; awasunge Hege mdindo wa mfumu wosungira akazi, nawapatse zowayeretsa;

4 ndi namwali womkonda mfumu akhale mkazi wamkuru m'malo mwa Vasiti. Ndipo cinthuci cinamkonda mfumu, nacita comweco.

5 Panali Myuda m'cinyumba ca ku Susani, dzina lace ndiye Moredekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi Mbenjamini;

6 uyu anatengedwa ndende ku Yerusalemu, pamodzi ndi andende anatengedwa pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda, amene Nebukadinezara mfumu ya Babulo adamtenga ndende.

7 Ndipo iye adalera Hadasa, ndiye Estere, mwana wamkazi wa atate wace wamng'ono; popeza iye analibe atate kapena amai; ndi namwaliyo anali wa maonekedwe okoma, ndi wokongola; ndipo atamwalira atate wace ndi mai wace, Moredekai anamtenga akhale mwana wace.

8 Ndipo kunali, atamveka mau a mfumu ndi lamulo lace, ndipo atasonkhanidwa anamwali ambiri m'cinyumba ca ku Susani, awasunge Hege, anamtenga Estere yemwe, alowe m'nyumba ya mfumu, amsunge Hege wosunga akazi.

9 Ndipo namwaliyo anamkomera, namcitira cifundo; ndipo anafulumira kumpatsa zace zomyeretsa, ndi magawo ace, ndi anamwali asanu ndi awiri oyenera kumpatsa ocokera m'nyumba ya mfumu; ndipo anamsuntha iye ndi anamwali ace akhale m'malo okometsetsa m'nyumba ya akazi.

10 Estere sadaulula mtundu wace ndi cibale cace; pakuti Moredekai adamuuzitsa kuti asadziulule.

11 Ndi Moredekai akayendayenda tsiku ndi tsiku ku bwalo la nyumba ya akazi, kuti adziwe umo akhalira Estere, ndi cimene cidzamcitikira.

12 Kunafika tsono kulowa kwace kwa namwali ali yense, kuti alowe kwa mfumu Ahaswero, atamcitira monga mwa lamulo la akazi, miyezi khumi ndi iwiri; pakuti adafokwaniritsa masiku a mayeretsedwe ao motero, miyezi isanu ndi umodzi ndi mafuta a mure, ndi miyezi isanu ndi umodzi ndi zonunkhira bwino, ndi zoyeretsa akazi.

13 Ndipo namwali ali yense analowa kwa mfumu matero, ziri zonse anafuna anampatsa zocokera m'nyumba ya akazi, alowe nazo ku nyumba ya mfumu.

14 Madzulo ace analowamo, nabwera m'mawa mwace kumka ku nyumba yaciwiri ya akazi, amsunge Saasigazi mdindo wa mfumu, wosunga akazi ang'ono a mfumu; iyeyu sanakwanso kwa mfumu, koma akakondwera naye mfumu, ndi kumuitana kumchula dzina lace, ndiko.

15 Pofika tsono kulowa kwace kwa Estere mwana wa Abihaili, atate wamng'ono wa Moredekai, amene adadzitengera akhale mwana wace, kuti alowe kwa mfumu, sanafuna kanthu koma zonena Hege mdindo wa mfumu wosunga akazi ndizo. Ndipo Estere anayamikizidwa pamaso pa onse ompenya.

16 Momwemo anatengedwa Estere kumka kwa mfumu Ahaswero, ku nyumba yace yacifumu, mwezi wakhumi, ndiwo mwezi wa Tebete, caka cacisanu ndi ciwiri ca ufumu wace.

17 Ndipo mfumu inakonda Estere koposa akazi onse, nalandira iye kuyanja ndi cifundo pamaso pace, koposa anamwali onse; motero anaika korona wacifumu pamutu pace, namuyesa mkazi wamkuru m'malo mwa Vasiti.

18 Pamenepo mfumu inawakonzera madyerero akuru ace onse, ndi omtumikira, ndiwo madyerero a Estere; napumulitsa maiko, naninkha zaufulu monga mwa ufulu wa mfumu.

19 Ndipo posonkhanidwa anamwali nthawi yaciwiri Moredekai anali wa m'bwalo la mfumu.

20 Estere sadaulula cibale cace kapena mtundu wace, monga Moredekai adamuuza; popeza Estere anacita mau a Moredekai monga m'mene analeredwa naye.

Moredekai aulula ciwembu cofuna kupha mfumu

21 Masiku awa pokhala Moredekai wa m'bwalo la mfumu, Bigitana ndi Teresi, adindo awiri a mfumu osunga pakhomo, anapsa mtima, nayesa kumthira manja mfumu Ahaswero.

22 Koma cidadziwika ici kwa Moredekai, ndiye anafotokozera Estere mkazi wamkuru; ndi Estere anamuuza mfumu, kumnenera Moredekai.

23 Ndipo atafunsira mlanduwo, anaupeza momwemo, napacikidwa onse awiri pamtengo; ndipo anacilemba m'buku la mbiri pamaso pa mfumu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10