1 Ndipo mfumu Ahaswero inasonkhetsa dziko, ndi zisumbu za ku nyanja yamcere.
2 Ndi zocita zonse za mphamvu yace, ndi nyonga zace, ndi mafotokozedwe a ukulu wa Moredekai, umene mfumu inamkulitsa nao, sizilembedwa kodi m'buku la mbiri ya mafumu a Mediya ndi Perisiya?
3 Pakuti Moredekai Myuda anatsatana naye mfumu Ahaswero, nakhala wamkuru mwa Ayuda, nabvomerezeka mwa unyinji wa abale ace wakufunira a mtundu wace zokoma, ndi wakunena za mtendere kwa mbeu yace yonse.