Estere 9 BL92

Ayuda awapha adani ao

1 Mwezi wakhumi ndi ciwiri tsono, ndiwo mwezi wa Adara, tsiku lace lakhumi ndi citatu, mau a mfumu ndi lamulo lace ali pafupi kucitika, tsikuli adani a Ayuda anayesa kuwacitira ufumu, koma cinasinthika; popeza Ayuda anacitira ufumu iwo odana nao;

2 pakuti Ayuda anasonkhana pamodzi m'midzi mwao, m'maiko onse a mfumu Ahaswero, kuwathira manja ofuna kuwacitira coipa, ndipo palibe munthu analimbika pamaso pao; popeza kuopsa kwao kudawagwera mitundu yonse ya anthu.

3 Ndipo akalonga onse a maikowo, ndi akazembe, ndi ziwanga, ndi iwo ocita nchito ya mfumu, anathandiza Ayuda; popeza kuopsa kwa Moredekai kudawagwera.

4 Pakuti Moredekai anali wamkuru m'nyumba ya mfumu, ndi mbiri yace idabuka m'maiko onse; pa kuti munthuyu Moredekai anakula-kulabe.

5 Ndipo Ayuda anakantha adani ao onse, kuwakantha ndi lupanga, ndi kuwapulula, nacitira odana nao monga anafuna.

6 Ndipo m'cinyumba ca ku Susani Ayuda anakantha, naononga amuna mazana asanu.

7 Napha Parisandata, ndi Dalifoni, ndi Asipata,

8 ndi Porata, ndi Adaliya, ndi Aridata,

9 ndi Parimasta, ndi Arisai, ndi Aridai, ndi Vaisata,

10 ana amuna khumi a Hamani mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalanda zofunkha.

11 Tsiku lomwelo anabwera naco kwa mfumu ciwerengo ca iwo ophedwa m'cinyumba ca ku Susani.

12 Ndipo mfumu inati kwa mkazi wamkuru Estere, Ayuda adapha, naononga amuna mazana asanu m'cinyumba ca ku Susani, ndi ana amuna khumi a Hamani; nanga m'maiko ena a mfumu munacitikanji? pempho lanu ndi ciani tsono? lidzacitikira inu; kapena mufunanjinso? kudzacitika.

13 Nati Estere, Cikakomera mfumu, alole Ayuda okhala m'Susani acite ndi mawa lomwe monga mwa lamulo la lero; ndi ana amuna khumi a Hamani apacikidwe pamtengo.

14 Ndipo mfumu inati azicita motero, nalamulira m'Susani, napacikidwa ana amuna khumi a Hamani.

15 Ndipo Ayuda okhala m'Susani anasonkhana pamodzi, tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi wa Adara, napha amuna mazana atatu m'Susani; koma sanalanda zofunkha.

16 Nasonkhana pamodzi Ayuda ena okhala m'maiko a mfumu, nalimbikira moyo wao, napumula pa adani ao, nawapha a iwo odana nao zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu; koma sanalanda zofunkha.

17 Cinacitika ici tsiku lakhumi ndi citatu la mwezi wa Adara, ndi tsiku lace lakhumi ndi cinai anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwesa.

18 Koma Ayuda okhala m'Susani anasonkhana tsiku lace lakhumi ndi citatu ndi lakhumi ndi cinai, ndi pa tsiku lakhumi ndi cisanu anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera.

19 Cifukwa cace Ayuda a kumiraga, okhala m'midzi yopanda malinga, amaliyesa tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi wa Adara tsiku la kukondwera ndi madyerero, ndi tsiku lokoma, ndi lakutumizirana magawo.

Masungidwe a tsiku la Purimu

20 Ndipo Moredekai analembera izi, natumiza akalata kwa Ayuda onse okhala m'maiko onse a mfumu Ahaswero, a kufupi ndi a kutali,

21 kuwalimbikitsira, asunge tsiku lakhumi ndi cinai, mwezi wa Adara, ndi tsiku lace lakhumi ndi cisanu lomwe, caka ndi caka,

22 ndiwo masiku amene Ayuda anapumula pa adani ao; ndi mwezi wacisoni unawasandulikira wakukondwera, ndi wamaliro ukhale tsiku lokoma, awayese masiku amadyerero ndi akukondwera, akutumizirana magawo, ndi akupatsa zaufulu kwa osauka.

23 Ndipo Ayuda anabvomereza kucita monga umo adayambira, ndi umo Moredekai adawalembera;

24 popeza Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda onse, adapangira Ayuda ciwembu kuwaononga, naombeza Puri, ndiwo ula, kuwatha ndi kuwaononga;

25 koma pofika mlanduwo kwa mfumu, anati mwa akalata kuti ciwembu cace coipa adacipangira Ayuda, cimbwerere mwini; ndi kuti Iye ndi ana amuna ace apacikidwe pamtengo,

26 Cifukwa cace anacha masikuwa Purimu, ndilo dzina la ulawo. Momwemo, cifukwa ca mau onse a kalatayo, ndi izi adaziona za mlanduwo, ndi ici cidawadzera,

27 Ayuda anakhazikitsa ici, nadzilonjezetsa okha, ndi mbeu yao, ndi onse akuphatikana nao, cingalekeke, kuti adzasunga masiku awa awiri monga mwalembedwa, ndi monga mwa nyengo yao yoikika, caka ndi caka;

28 ndi kuti masikuwa adzakumbukika ndi kusungika mwa mibadwo yonse, banja liri lonse, dziko liri lonse, ndi mudzi uli wonse; ndi kuti masiku awa sadzalekeka mwa Ayuda, kapena kusiyidwa cikumbukilo cao mwa mbeu yao.

29 Pamenepo Estere mkazi wamkuru mwana wa Abihaili, ndi Moredekai Myuda, analembera molamulira, kukhazikitsa kalata uyu waciwiri wa Purimu.

30 Natumiza iye akalata kwa Ayuda onse, ku maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri a ufumu wa Ahaswero, ndiwo mau a mtendere ndi coonadi;

31 kukhazikitsa masiku awa a Purimu m'nyengo zao, m'mene Moredekai Myuda ndi mkazi wamkuru Estere adawakhazikitsira; ndi umo anadzikhazikitsira okha, ndi mbeu yao, kunena za kusala kwao, ndi kupfuula kwao.

32 Ndipo kunena kwace kwa Estere kunakhazikitsa mau awa a Purimu; ndipo kunalembedwa m'buku.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10