1 Tsiku lomwelo mfumu Ahaswero anampatsa mkazi wamkuru Estere nyumba ya Hamani mdani wa Ayuda, Nafika Moredekai pamaso pa mfumu; pakuti Estere adamuuza za cibale cace.
2 Ndipo mfumu inabvula mphete yace adailanda kwa Hamani, naipereka kwa Moredekai. Ndi Estere anaika Moredekai akhale woyang'anira nyumba ya Hamani.
3 Nanenanso Estere pamaso pa mfumu, nagwa ku mapazi ace, nalira misozi, nampembedza kuti acotse coipaco ca Hamani wa ku Agagi, ndi ciwembu adacipangira Ayuda,
4 Ndipo mfumu inaloza Estere ndi ndodo yacifumu yagolidi. Nanyamuka Estere, naima pamaso pa mfumu.
5 Nati, Cikakomera mfumu, ndipo ngati yandikomera mtima, niciyenera kwa mfumu, ngatinso ndimcititsa kaso, alembere cosintha mau a akalata a ciwembu ca Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, amene adawalembera kuononga Ayuda okhala m'maiko onse a mfumu;
6 pakuti ndidzapirira bwanji pakuciona coipa cirikudzera amtundu wanga, kapena ndidzapirira bwanji pakuciona cionongeko ca pfuko langa?
7 Pamenepo mfumu Ahaswero anati kwa mkazi wamkuru Estere, ndi kwa Moredekai Myuda, Taonani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndi iyeyu anampacika pamtanda, cifukwa anaturutsa dzanja lace pa Avuda,
8 Mulembere inunso kwa Ayuda monga mufuna, m'dzina la mfumu, nimusindikize ndi mphete ya mfumu; pakuti kalata wolembedwa m'dzina la mfumu, ndi kusindikizika ndi mphete ya mfumu, palibe munthu akhoza kumsintha.
9 Pamenepo anaitana alembi a mfumu nthawi yomweyo, mwezi wacitatu, ndiwo mwezi wa Sivani, tsiku lace la makumi awiri ndi citatu, monga mwa zonse Moredekai analamulira; nalembera kwa Ayuda ndi kwa akazembe, ndi ziwanga, ndi akalonga a kumaiko, oyambira ku Indiya, ofikira ku Kusi, maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri, ku dziko liri lonse monga mwa cilembedwe cao, ndi mtundu uli wonse monga mwa cinenedwe cao, ndi kwa Ayuda monga mwa cilembedwe cao, ndi monga mwa cinenedwe cao.
10 Ndipo analembera m'dzina la mfumu Ahaswero, nasindikiza ndi mphete ya mfumu, natumiza akalata ndi amtokoma pa akavalo, okwera pa akavalo aliwiro acifumu, obadwa mosankhika;
11 m'menemo mfumu inalola Ayuda okhala m'midzi iri yonse asonkhane, ndi kulimbikira moyo wao, kuononga, kupha, ndi kupulula mphamvu yonse ya anthu ndi ya dziko yofuna kuwathira nkhondo, iwo, ana ang'ono ao, ndi akazi ao, ndi kulanda zofunkha zao,
12 tsiku lomwelo, m'maiko onse a mfumu Ahaswero, tsiku lakhumi ndi citatu la mwezi wakhumi ndi ciwiri, ndiwo mwezi wa Adara.
13 Citsanzo cace, ca lemboli, cakuti abukitse lamulo m'maiko onse, cinalalikidwa kwa mitundu yonse ya anthu, kuti, Ayuda akonzekeretu tsiku lijalo, kubwezera cilango adani ao.
14 Naturuka amtokoma okwera pa akavalo aliwiro acifumu; pakuti mau a mfumu anawafulumiza ndi kuwaumiriza; ndipo lamulolo linabukitsidwa m'cinyumba ca ku Susani.
15 Ndipo Moredekai anaturuka pamaso pa mfumu wobvala cobvala cacifumu camadzi ndi coyera, ndi korona wamkuru wagolidi, ndi maraya abafuta ndi ofiirira; ndi mudzi wa Susani unapfuula ndi kukondwera.
16 Ayuda anali nako kuunika, ndi kukondwera, ndi cimwemwe, ndi ulemu.
17 Ndi m'maiko monse, ndi m'midzi yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lace, Ayuda anali nako kukondwera ndi cimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m'dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera.