1 Motero inadza mfumu ndi Hamani kumwa naye mkazi wamkuru Estere.
2 Nitinso mfumu kwa Estere tsiku laciwirili pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nciani, mkazi wamkuru Estere? lidzapatsidwa kwa inu; mufunanji? cidzacitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumu wanga.
3 Nayankha mkazi wamkuru Estere, nati, Ngati mwandikomera mtima, mfumu, ndipo cikakomera mfumu, andilekere moyo wanga pa kupempha kwanga, ndi wa anthu a mtundu wanga pa pempho langa;
4 pakuti tagulitsidwa; ine ndi anthu amtundu wanga, kuti ationonge, atiphe, natipulule, Koma tikadagulitsidwa tikhale akapolo ndi adzakazi, ndikadakhala cete; cinkana wosautsa sakadakhoza kubwezera kusowa kwa mfumu.
5 Pamenepo mfumu Ahaswero inalankhula, niti kwa mkazi wamkuru Estere, Ndani uyu, ali kuti iyeyu wadzazidwa mtima wace kuti azitero?
6 Nati Estere, Munthu wosautsa ndi mdani ndiye Hamani woipa uyu. Pamenepo Hamani anagwidwa mantha pamaso pa mfumu ndi mkazi wamkuru.
7 Ninyamuka mfumu mu mkwiyo wace ku madyerero a vinyo, nimka ku munda wa maluwa wa kucinyumba; koma Hamani anatsalira kudzipempherera moyo kwa mkazi wamkuru Estere; popeza anapenya kuti mfumu inatsimikiza mtima kumcitira coipa.
8 Nibwera mfumu ku munda wa maluwa wa kucinyumba kulowanso m'nyumba munali madyerero a vinyo, napeza Hamani atagwa pa kama wokhalapo Estere. Niti mfumu, Kodi aumiriza mkazi wamkuru pamaso panga m'nyumba? Poturuka mau pakamwa pa mfumu anamphimba Hamani nkhope.
9 Nati Haribona wina wa adindo okhala pamaso pa mfumu, Taonaninso, mtengowo msinkhu wace mikono makumi asanu, umene Hamani anaupangira Moredekai wonenera mfumu zokoma, uimiritsidwa m'nyumba ya Hamani. Niti mfumu, Mpacike pomwepo.
10 Nampacika Hamani pa mtengo adaukonzera Moredekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.