1 Zitatha izi, mfumu Ahaswero anamkuza Hamani mwana wa Hamedata, wa ku Agagi, namkweza, naika mpando wace upose akalonga onse okhala naye.
2 Ndipo anyamata onse a mfumu okhala m'cipata ca mfumu anamweramira, namgwadira Hamani; pakuti mfumu idalamulira cotero za iye. Koma Moredekai sanamweramira kapena kumgwadira.
3 Ndipo anyamata a mfumu okhala m'cipata ca mfumu anati kwa Moredekai, Ulakwiranji pa lamulo la mfumu?
4 Kunali tsono, pomalankhula naye tsiku ndi tsiku, osawamvera iye, anauza Hamani, kuona ngati mlandu wa Moredekai udzakoma; popeza iye adawauza kuti ali Myuda.
5 Ndipo Hamani, pakuona kuti Moredekai sanamweramira kapena kumgwadira, mtima wace unadzala mkwiyo.
6 Koma anaciyesa copepuka kumthira manja Moredekai yekha; pakuti adamfotokozera mtundu wace wa Moredekai; potero Hamani anafuna kuononga Ayuda lonse okhala m'ufumu wonse wa Ahaswero, ndiwo a mtundu wa Moredekai.
7 Mwezi woyamba ndiwo mwezi wa Nisani, caka cakhumi ndi ciwiri ca mfumu Ahaswero, anaombeza Puri, ndiwo ula, pamaso pa Hamani tsiku ndi tsiku, mwezi ndi mwezi, mpaka mwezi wakhumi ndi ciwiri, ndiwo mwezi wa Adara.
8 Ndipo Hamani anati kwa mfumu Ahaswero, Pali mtundu wina wa anthu obalalika ndi ogawanikana mwa mitundu ya anthu m'maiko onse a ufumu wanu, ndi malamulo ao asiyana nao a anthu onse, ndipo sasunga malamulo a mfumu; cifukwa cace mfumu siiyenera kuwaleka.
9 Cikakomera mfumu, cilembedwe kuti aonongeke iwo; ndipo ndidzapereka matalente a siliva zikwi khumi m'manja a iwo akusunga nchito ya mfumu, abwere nao kuwaika m'nyumba za cuma ca mfumu.
10 Ndipo mfumu inabvula mphete yace pa cala cace, naipereka kwa Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda.
11 Ndipo mfumu idati kwa Hamani, Siliva akhale wako, ndi anthu omwe; ucite nao monga momwe cikukomera.
12 Pamenepo anaitana alembi a mfumu mwezi woyamba, tsiku lace lakhumi ndi citatu, nalembera monga mwa zonse Hamani analamulira akazembe ndi ziwanga zoyang'anira maiko ali onse, ndi akalonga a mitundu iri yonse ya anthu, maiko ali onse monga mwa cilembedwe cao, ndi mitundu iri yonse ya anthu monga mwa cinenedwe cao; anazilemba m'dzina la mfumu Ahaswero, nazisindikiza ndi mphete ya mfumu.
13 Ndipo anatumiza akalata ndi amtokoma ku maiko onse a mfumu, kuti aononge, aphe, napulule Ayuda onse, ndiwo ana, ndi okalamba, makanda, ndi akazi, tsiku limodzi, ndilo tsiku lakhumi ndi citatu la mwezi wakhumi ndi ciwiri, ndiwo mwezi wa Adara; nalande zao mofunkha.
14 Mau a colembedwaco, ndiwo kuti licitike lamulo m'maiko onse, analalikidwa kwa anthu onse, kuti akonzekeretu tsiku lomwelo.
15 Amtokoma anaturuka ofulumizidwa ndi mau a mfumu, ndi lamulo linabukitsidwa m'cinyumba ca ku Susani; ndipo mfumu ndi Hamani anakhala pansi kumwa; koma mudzi wa Susani unadodoma.