1 Koma podziwa Moredekai zonse zidacitikazi, Moredekai anang'amba zobvala zace, nabvala ciguduli ndi mapulusa, naturuka pakati pa mudzi, napfuula, nalira kulira kwakukuru ndi kowawa,
2 nafika popenyana ndi cipata ca mfumu; popeza sanathe munthu kulowa ku cipata ca mfumu wobvala ciguduli.
3 Ndi m'maiko monse, pali ponse anafikapo mau a mfumu ndi lamulo lace, panali maliro akuru mwa Ayuda, ndi kusala, ndi kulira misozi, ndi kubuma; nagona m'ciguduli ndi mapulusa ambiri.
4 Ndipo anamwali a Estere ndi adindo ace anadza, namuuza; ndi mkazi wamkuru anawawidwa mtima kwambiri, natumiza cobvala abveke Moredekai, ndi kumcotsera ciguduli cace; koma sanacilandira.
5 Pamenepo Estere anaitana Hataki mdindo wina wa mfumu, amene idamuika amtumikire, namuuza amuke kwa Moredekai, kuti adziwe ici nciani ndi cifukwa cace ninji.
6 Naturuka Hataki kumka kwa Moredekai ku khwalala la mudzi linali popenyana ndi cipata ca mfumu.
7 Ndipo Moredekai anamfotokozera zonse zidamgwera, ndi mtengo wace wa ndarama adati Hamani adzapereka m'nyumba ya cuma ca mfumu pa Ayuda, kuwaononga.
8 Anampatsanso citsanzo ca lamulo lolembedwa adalibukitsa m'Susani, kuwaononga, acionetse kwa Estere, ndi kumfotokozera, ndi kumlangiza alowe kwa mfumu, kumpembedza, ndi kupempherera anthu ace kwa iye.
9 Nadza Hataki, namuuza Estere mau a Moredekai.
10 Pamenepo Estere ananena ndi Hataki, namtuma akauze Moredekai, ndi kuti,
11 Akapolo onse a mfumu ndi anthu a m'maiko a mfumu adziwa kuti ali yense, ngakhale wamwamuna kapena wamkazi, akalowa kwa mfumu ku bwalo la m'katimo wosaitanidwa, lamulo la pa iye ndi limodzi, ndilo kuti amuphe, akapanda mfumu kumloza ndi ndodo yacifumu yagolidi kuti akhale ndi moyo; koma ine sanaodiitana ndilowe kwa mfumu masiku awa makumi atatu.
12 Ndipo anamuuza Moredekai mau a Estere.
13 Koma Moredekai anawauza ambwezere mau Estere, kuti, Usamayesa m'mtima mwako kuti udzapulumuka m'nyumba ya mfumu koposa Ayuda onse ena.
14 Pakuti ukakhala cete konse tsopano lino, cithandizo ndi cipulumutso zidzafuma kwina; koma iwe ndi nyumba ya atate wako mudzaonongeka; ndipo kaya, kapena walowera ufumu cifukwa ca nyengo yonga iyi.
15 Pamenepo Estere anati ambwezere mau Moredekai,
16 Muka, sonkhanitsa Ayuda onse opezeka m'Susani, nimundisalire, osadya osamwa masiku atatu, usiku ndi usana, ine ndemwe ndi anamwali anga tidzasala momwemo, ndipo motero ndidzalowa kwa mfumu, ndiko kosalingana ndi lamulo; ndikaonongeka tsono ndionongeke,
17 Napita Moredekai, nacita monga mwa zonse adamlamulira Estere.