3 Niti mfumu, Anamcitira Moredekai ulemu ndi ukulu wotani cifukwa ca ici? Ndipo anyamata a mfumu akuitumikira ananena nayo, Sanamcitira kanthu.
4 Niti mfumu, Ali kubwalo ndani? Koma Hamani adalowa m'bwalo lakunja la nyumba ya mfumu kulankhula ndi mfumu za kupacika Moredekai pamtengo adaukonzeratu.
5 Ndipo anyamata a mfumu ananena nayo, Taonani, Hamani alikuima pabwalo. Niti mfumu, Alowe.
6 Nalowa Hamani. Ndipo mfumu inati kwa iye, Kodi amcitire ciani munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu? Ndipo Hamani anati mumtima mwace, Ndaniyo mfumu ikondwera kumcitira ulemu koposa ine?
7 Nati Hamani kwa mfumu, Munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu,
8 amtengere cobvala cacifumu amacibvala mfumu, ndi kavalo amakwerapo mfumu, naike korona wacifumu pamutu pace,
9 napereke cobvala ndi kavalo m'dzanja la wina womveketsa wa akalonga a mfumu, nabveke naco munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu, namuyendetse pa kavaloyo m'khwalala la m'mudzi, napfuule pamaso pace, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu.