2 Ndipo mfumu inabvula mphete yace adailanda kwa Hamani, naipereka kwa Moredekai. Ndi Estere anaika Moredekai akhale woyang'anira nyumba ya Hamani.
3 Nanenanso Estere pamaso pa mfumu, nagwa ku mapazi ace, nalira misozi, nampembedza kuti acotse coipaco ca Hamani wa ku Agagi, ndi ciwembu adacipangira Ayuda,
4 Ndipo mfumu inaloza Estere ndi ndodo yacifumu yagolidi. Nanyamuka Estere, naima pamaso pa mfumu.
5 Nati, Cikakomera mfumu, ndipo ngati yandikomera mtima, niciyenera kwa mfumu, ngatinso ndimcititsa kaso, alembere cosintha mau a akalata a ciwembu ca Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, amene adawalembera kuononga Ayuda okhala m'maiko onse a mfumu;
6 pakuti ndidzapirira bwanji pakuciona coipa cirikudzera amtundu wanga, kapena ndidzapirira bwanji pakuciona cionongeko ca pfuko langa?
7 Pamenepo mfumu Ahaswero anati kwa mkazi wamkuru Estere, ndi kwa Moredekai Myuda, Taonani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndi iyeyu anampacika pamtanda, cifukwa anaturutsa dzanja lace pa Avuda,
8 Mulembere inunso kwa Ayuda monga mufuna, m'dzina la mfumu, nimusindikize ndi mphete ya mfumu; pakuti kalata wolembedwa m'dzina la mfumu, ndi kusindikizika ndi mphete ya mfumu, palibe munthu akhoza kumsintha.